Werenga Madalitso ako

 

Pamene zovuta za dziko zazinga
Pamene wakhumudwa zonse zataika
Werenga zabwino zomwe uli nazo
Ndipo udzazindikira mbuye ngokoma


Ref
Werenga Madalitso ako, Utchule limodzi limodzi,
Werenga Madalitso ako, Ona zimene Mulungu wakuchitira


Kodi walemedwa ndi zovuta zadziko
Kapena mtanda wako ukulemera
Werenga zabwino zomwe uli nazo
Ndipo udzaimba nyimbo yomutamanda


Tsopano pakati pamavuto ako
Usataye mtima Mulungu akuona
Ganiza zabwino zomwe wakuchitira
Adzakugwira dzanja ulendo onsewo

https://youtu.be/eQFfdCLUohc

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *