Thanthwe Long’ambikatu

 


1.Thanthwe Long’ambikatu, ndibisale momwemu!
Madzi ndipo mwaziwo zuturuka m’nthitimo,
Zinditsuke m’mtima mbu, Zindilimbikitsetu.


2.Ntchito zanga zonsezo sidikondweretsa ‘Nu,
Ndikazigwiritsadi, ndikhalira nsonizi,
Zonse sizikwanazi, koma Yesu yekhayo.


3. M’manja mwanga chabe bi, mtanda ndingogwiradi;
‘Maliseche mveke ‘ne, ndiri ndekha nsunge ‘ne,
Ndithawire mtsinjewo, mundisunge m’mtimamo.


4.M’moyo uno kunsiku, pena ndimwaliratu,
Ndi kufika kwanuko, tionane masowo;
Thanthwe Long’ambikatu, ndibisale momwemu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *